Surah Yaseen Ndi Chomasuliridwa mu Chinyanja
Surah Yaseen yomasulira kwa Nyanja ili ndi zokhudzira zambiri zauzimu ndi malingaliro pa moyo wa munthu. Ndi mutu wa 36 wa Qur’an yopatulika, yopezeka mu Para 22 ndi 23 ya Quran. Surayi Yaseen ili ndi chiongoko champhamvu ndi nzeru. Kuwerenga kumasulira kwake kumathandiza Asilamu kumvetsa bwino uthenga wake, kuwonjezera chidziwitso ndi kupangitsa kuti ziphunzitso zake zikhale zatanthauzo. Limaperekanso maphunziro a makhalidwe abwino omwe amamveketsa bwino moyo watsiku ndi tsiku.
Ndime 83 za Surah Yaseen zingabweretse mtendere wamumtima, makamaka panthawi yamavuto. Ngakhale kulibwereza mu Chiarabu kumabweretsa mphotho yauzimu, kumvetsetsa tanthauzo lathunthu kudzera mu kumasulira kumalola kulumikizana mwakuya. Surah Yaseen ikupezeka m’zilankhulo 95+, zomwe zimapangitsa kuti anthu padziko lonse lapansi azipezeka. Msilamu aliyense akulimbikitsidwa kuwerenga Baibulo lonselo kamodzi kokha kuti amvetse bwino uthenga wake. Ndikosavuta kwa owerenga kunena mawu a Surah Yaseen pa intaneti kapena kukopera Surah Yaseen Nyanja PDF yonse ndi kuisunga kuzipangizo zawo kuti aipeze mwachangu—ngakhale popanda intaneti.
Listen Surah Yaseen Nyanja Audio
Funda Surah Yaseen Yonse ndi Tanthauzo la Chinyanja pa Intaneti
36.7
لَقَدۡ حَقَّ ٱلۡقَوۡلُ عَلَىٰٓ أَكۡثَرِهِمۡ فَهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ
Ndithu, mawu (onena za chilango) Atsimikizika pa ambiri a iwo; Poti iwo sakhulupirira.ا
Tafseer
36.6
لِتُنذِرَ قَوۡمٗا مَّآ أُنذِرَ ءَابَآؤُهُمۡ فَهُمۡ غَٰفِلُونَ
Kuti uwachenjeze anthu omwe atate Awo sadachenjezedwe; choncho iwo Ngoiwala.ا
Tafseer
36.9
وَجَعَلۡنَا مِنۢ بَيۡنِ أَيۡدِيهِمۡ سَدّٗا وَمِنۡ خَلۡفِهِمۡ سَدّٗا فَأَغۡشَيۡنَٰهُمۡ فَهُمۡ لَا يُبۡصِرُونَ
Ndipo tawaikira Chotsekereza patsogolo pawo ndi Chotsekereza pambuyo pawo, Ndipo maso awo tawaphimba, tero Iwo saona.ا
Tafseer
36.8
إِنَّا جَعَلۡنَا فِيٓ أَعۡنَٰقِهِمۡ أَغۡلَٰلٗا فَهِيَ إِلَى ٱلۡأَذۡقَانِ فَهُم مُّقۡمَحُونَ
Ndithu Ife taika magoli m’makosi Mwawo ofika kuzibwano, kotero kuti Mitu yawo yayang’ana mmwamba; (Siingathe kutembenuka ndi kuyang’ana).ا
Tafseer
36.11
إِنَّمَا تُنذِرُ مَنِ ٱتَّبَعَ ٱلذِّكۡرَ وَخَشِيَ ٱلرَّحۡمَٰنَ بِٱلۡغَيۡبِۖ فَبَشِّرۡهُ بِمَغۡفِرَةٖ وَأَجۡرٖ كَرِيمٍ
Ndithu, kuchenjeza kwako Kupindulira amene watsatira Qur’an ndi kumuopa Wachifundo ngakhale sakumuona. Wotere muuze nkhani yabwino ya Chikhululuko ndi malipiro aulemu.ا
Tafseer
36.10
وَسَوَآءٌ عَلَيۡهِمۡ ءَأَنذَرۡتَهُمۡ أَمۡ لَمۡ تُنذِرۡهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ
Ndipo kwa iwo nchimodzimodzi, Uwachenjeze ngakhale usawachenjeze Sangakhulupirire.ا
Tafseer
36.13
وَٱضۡرِبۡ لَهُم مَّثَلًا أَصۡحَٰبَ ٱلۡقَرۡيَةِ إِذۡ جَآءَهَا ٱلۡمُرۡسَلُونَ
Ndipo atchulire, Nkhani ya eni mudzi pamene Atumiki adaudzera mudziwo.ا
Tafseer
36.12
إِنَّا نَحۡنُ نُحۡيِ ٱلۡمَوۡتَىٰ وَنَكۡتُبُ مَا قَدَّمُواْ وَءَاثَٰرَهُمۡۚ وَكُلَّ شَيۡءٍ أَحۡصَيۡنَٰهُ فِيٓ إِمَامٖ مُّبِينٖ
Ndithu, Ife tidzaukitsa akufa, Ndipo tikulemba zimene atsogoza (M’dziko lapansi m’zochita zawo) Ndi zomwe amasiya pambuyo , ndipo Chinthu chilichonse tachilemba M’kaundula wopenyeka (wofotokoza Chilichonse).ا
Tafseer
36.15
قَالُواْ مَآ أَنتُمۡ إِلَّا بَشَرٞ مِّثۡلُنَا وَمَآ أَنزَلَ ٱلرَّحۡمَٰنُ مِن شَيۡءٍ إِنۡ أَنتُمۡ إِلَّا تَكۡذِبُونَ
(Eni mudzi) adati: “Inu ndi anthu Ngati ife; (Mulungu) Wachifundo Chambiri sadavumbulutse chilichonse; inu simuli kanthu koma Mukunena bodza.”ا
Tafseer
36.14
إِذۡ أَرۡسَلۡنَآ إِلَيۡهِمُ ٱثۡنَيۡنِ فَكَذَّبُوهُمَا فَعَزَّزۡنَا بِثَالِثٖ فَقَالُوٓاْ إِنَّآ إِلَيۡكُم مُّرۡسَلُونَ
Pamene tidatumiza atumiki awiri kwa Iwo adawatsutsa; ndipo tidawalimbika Iwo (awiriwo) potumiza wachitatu. (Atumiki atatuwo) adati: “Ife Tatumidwa kwa inu.”ا
Tafseer
36.17
وَمَا عَلَيۡنَآ إِلَّا ٱلۡبَلَٰغُ ٱلۡمُبِينُ
Ndipo palibe china pa ife, koma Kufikitsa kwachimvekere uthenga (Wa Mulungu).”ا
Tafseer
36.16
قَالُواْ رَبُّنَا يَعۡلَمُ إِنَّآ إِلَيۡكُمۡ لَمُرۡسَلُونَ
(Atumiki) adati: “Mbuye wathu (Amene watituma kwa inu) akudziwa Kuti ife ndi otumidwadi kwa inu.ا
Tafseer
36.19
قَالُواْ طَـٰٓئِرُكُم مَّعَكُمۡ أَئِن ذُكِّرۡتُمۚ بَلۡ أَنتُمۡ قَوۡمٞ مُّسۡرِفُونَ
(Atumiki) adati: “Tsoka lanu Lili ndi inu (chifukwa Cha kukana kwanu ndi kupitiriza Kupembedza mafano). Kodi Mukakumbutsidwa Koma inu ndi anthu olumpha malire”.ا
Tafseer
36.18
قَالُوٓاْ إِنَّا تَطَيَّرۡنَا بِكُمۡۖ لَئِن لَّمۡ تَنتَهُواْ لَنَرۡجُمَنَّكُمۡ وَلَيَمَسَّنَّكُم مِّنَّا عَذَابٌ أَلِيمٞ
(Eni mudzi) adati: “Ife tapeza Tsoka chifukwa cha inu: Ngati Simusiya Tikugendani ndi miyala; ndipo Kuchokera kwa ife chikupezani.ا
Tafseer
36.21
ٱتَّبِعُواْ مَن لَّا يَسۡـَٔلُكُمۡ أَجۡرٗا وَهُم مُّهۡتَدُونَ
Atsateni omwe sakupemphani malipiro (Pakukulangizani kwawo), Ndipo iwo ngoongoka.ا
Tafseer
36.20
وَجَآءَ مِنۡ أَقۡصَا ٱلۡمَدِينَةِ رَجُلٞ يَسۡعَىٰ قَالَ يَٰقَوۡمِ ٱتَّبِعُواْ ٱلۡمُرۡسَلِينَ
Kenako munthu adadza akuthamanga Kuchokera kumalekezero a mzindawo (Ndipo) adati: “E, inu anthu anga! Atsateni atumikiwa.ا
Tafseer
36.23
أَأَتَّخِذُ مِنْ دُونِهِ آلِهَةً إِنْ يُرِدْنِ الرَّحْمَٰنُ بِضُرٍّ لَا تُغْنِ عَنِّي شَفَاعَتُهُمْ شَيْئًا وَلَا يُنْقِذُونِ
Kodi ndidzipangire milungu Kusiya lye (Mulungu) ? Chipulumutso chawo Sichingandipindulire chilichonse Ngati (Mulungu) Wachifundo Chambiri atafuna kundichitira Zoipa; Ndipo siingandipulumutse.ا
Tafseer
36.22
وَمَا لِيَ لَآ أَعۡبُدُ ٱلَّذِي فَطَرَنِي وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ
Kodi nchiyani chingandiletse ine Kupembedza Yemwe adandilenga? Ndipo kwa lye ndi komwe inu nonse Mudzabwerera.ا
Tafseer
36.27
بِمَا غَفَرَ لِي رَبِّي وَجَعَلَنِي مِنَ الْمُكْرَمِينَ
Momwe Mbuye wanga wandikhululukira Ndikundichita kukhala mmodzi wa Opatsidwa ulemu (akadakhulupirira)”ا
Tafseer
36.26
قِيلَ ادْخُلِ الْجَنَّةَ ۖ قَالَ يَا لَيْتَ قَوْمِي يَعْلَمُونَ
Kudanenedwa (kwa iye): “Lowa M’munda wa Mtendere.” Iye adati: “Ha! Anthu anga, Akadadziwa!ا
Tafseer
36.29
إِنْ كَانَتْ إِلَّا صَيْحَةً وَاحِدَةً فَإِذَا هُمْ خَامِدُونَ
Kunangophulika kamodzi kokha ndipo zonse zinatheratu.ا
Tafseer
36.28
وَمَا أَنْزَلْنَا عَلَىٰ قَوْمِهِ مِنْ بَعْدِهِ مِنْ جُنْدٍ مِنَ السَّمَاءِ وَمَا كُنَّا مُنْزِلِينَ
Pambuyo pake, sitidawatumizire gulu lankhondo Lochokera kumwamba kuti likumane ndi anthu ake, ndipo sikudali kofunika kwa Ife kuwatumiza.ا
Tafseer
36.31
أَلَمْ يَرَوْا كَمْ أَهْلَكْنَا قَبْلَهُمْ مِنَ الْقُرُونِ أَنَّهُمْ إِلَيْهِمْ لَا يَرْجِعُونَ
Kodi sadalingalire za mibadwo Yambirimbiri imene tidaiononga Patsogolo pawo? Ndipo iwo Sangabwererenso kwa iwo?ا
Tafseer
36.30
يَا حَسْرَةً عَلَى الْعِبَادِ ۚ مَا يَأْتِيهِمْ مِنْ رَسُولٍ إِلَّا كَانُوا بِهِ يَسْتَهْزِئُونَ
Ha! Nzodandaulitsa kwa Anthu! Palibe pamene Mtumiki adawadzera popanda Kumchitira chipongwe (ndi kukana Kumtsata)!ا
Tafseer
36.33
وَآيَةٌ لَهُمُ الْأَرْضُ الْمَيْتَةُ أَحْيَيْنَاهَا وَأَخْرَجْنَا مِنْهَا حَبًّا فَمِنْهُ يَأْكُلُونَ
Ndipo chisonyezo chawo Ndi nthaka ya chilala; Timaiukitsa (ndi madzi) ndi kutulutsa M’menemo njere, Zomwe zina mwa izo amadya.ا
Tafseer
36.32
وَإِنْ كُلٌّ لَمَّا جَمِيعٌ لَدَيْنَا مُحْضَرُونَ
Ndipo zolengedwa zonse Zidzaonekera kwa Ife.ا
Tafseer
36.35
لِيَأْكُلُوا مِنْ ثَمَرِهِ وَمَا عَمِلَتْهُ أَيْدِيهِمْ ۖ أَفَلَا يَشْكُرُونَ
Kuti azidya zipatso zake pomwe Sizidapangidwe ndi manja awo. Kodi bwanji sathokoza (Mulungu)?ا
Tafseer
36.34
وَجَعَلْنَا فِيهَا جَنَّاتٍ مِنْ نَخِيلٍ وَأَعْنَابٍ وَفَجَّرْنَا فِيهَا مِنَ الْعُيُونِ
Ndipo tapanga m’menemo minda Ya kanjedza ndi mpesa; Ndipo tatulutsa m’menemo akasupe..ا
Tafseer
36.37
وَآيَةٌ لَهُمُ اللَّيْلُ نَسْلَخُ مِنْهُ النَّهَارَ فَإِذَا هُمْ مُظْلِمُونَ
Ndiponso chisonyezo chawo Ndiusiku. M’menemo timachotsamo Usana (womwe umabisa usiku), ndipo (Anthu) amangozindikira ali mumdima;ا
Tafseer
36.36
سُبْحَانَ الَّذِي خَلَقَ الْأَزْوَاجَ كُلَّهَا مِمَّا تُنْبِتُ الْأَرْضُ وَمِنْ أَنْفُسِهِمْ وَمِمَّا لَا يَعْلَمُونَ
Alemekezeke (Mulungu), Amene adalenga zinthu zonse, chachimuna ndi Chachikazi, kuchokera m’zimene Nthaka ikutulutsa, ndi iwo omwe Ndi zina zimene (anthu) sakudziwa.ا
Tafseer
36.39
وَالْقَمَرَ قَدَّرْنَاهُ مَنَازِلَ حَتَّىٰ عَادَ كَالْعُرْجُونِ الْقَدِيمِ
Ndipo mwezi (Tidauikira magawo ake) mpaka udzakhalanso ngati nthambi yakale youma ya kanjedza.ا
Tafseer
36.38
وَالشَّمْسُ تَجْرِي لِمُسْتَقَرٍّ لَهَا ۚ ذَٰلِكَ تَقْدِيرُ الْعَزِيزِ الْعَلِيمِ
Ndi Dzuwa: Likusunthira kumalo ake opumula. Ili ndi lamulo la Mulungu Wamphamvu zonse, Wodziwa zonse.ا
Tafseer
36.41
وَآيَةٌ لَهُمْ أَنَّا حَمَلْنَا ذُرِّيَّتَهُمْ فِي الْفُلْكِ الْمَشْحُونِ
Ndiponso pali chisonyezo kwa iwo. Ndithu, tidaukweza mtundu Wawo chombo chodzazidwa.ا
Tafseer
36.40
لَا الشَّمْسُ يَنْبَغِي لَهَا أَنْ تُدْرِكَ الْقَمَرَ وَلَا اللَّيْلُ سَابِقُ النَّهَارِ ۚ وَكُلٌّ فِي فَلَكٍ يَسْبَحُونَ
Nkosatheka kwa dzuwa kukumana ndi Mwezi; nawonso Usiku sungathe kupambana usana. Ndipo chilichonse Mwa izo chimasambira m’njira Yake.ا
Tafseer
36.43
وَإِنْ نَشَأْ نُغْرِقْهُمْ فَلَا صَرِيخَ لَهُمْ وَلَا هُمْ يُنْقَذُونَ
Ndipo ngati titafuna tikhoza kuwamiza M’madzi, ndipo sangapezeke Wowathandiza, ndiponso Sangapulumutsidwe.ا
Tafseer
36.42
وَخَلَقْنَا لَهُمْ مِنْ مِثْلِهِ مَا يَرْكَبُونَ
Kenako anawapangiranso ziwiya zina zofanana ndi zimenezi zimene amakweramo.ا
Tafseer
36.45
وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ اتَّقُوا مَا بَيْنَ أَيْدِيكُمْ وَمَا خَلْفَكُمْ لَعَلَّكُمْ تُرْحَمُونَ
Ndipo kukanenedwa kwa iwo: “Opani zomwe ziri patsogolo Panu ndi zomwe ziri Pambuyo panu kuti muchitiridwe Chifundo.”ا
Tafseer
36.44
إِلَّا رَحْمَةً مِنَّا وَمَتَاعًا إِلَىٰ حِينٍ
Koma (sitikuwamiza) chifukwa cha Chifundo Chathu pa iwo ndi kuti Asangalale kufikira nthawi yawo (Yofera).ا
Tafseer
36.47
وَإِذَا قِيلَ لَهُمْ أَنْفِقُوا مِمَّا رَزَقَكُمُ اللَّهُ قَالَ الَّذِينَ كَفَرُوا لِلَّذِينَ آمَنُوا أَنُطْعِمُ مَنْ لَوْ يَشَاءُ اللَّهُ أَطْعَمَهُ إِنْ أَنْتُمْ إِلَّا فِي ضَلَالٍ مُبِينٍ
Ndipo kukanenedwa kwa iwo: “Patsani (aumphawi) zimene Mulungu wakupatsani,” Osakhulupirira amanena kwa Okhulupirira: “Kodi tidyetse Yemwe Mulungu akadafuna Akadamdyetsa; ? Ndithu, inu simuli Kanthu koma muli m’kusokera Koonekeratu.”ا
Tafseer
36.46
وَمَا تَأْتِيهِمْ مِنْ آيَةٍ مِنْ آيَاتِ رَبِّهِمْ إِلَّا كَانُوا عَنْهَا مُعْرِضِينَ
Ndipo palibe chisonyezo chilichonse Mwazisonyezo za Mbuye wawo Chomwe chidawadzera popanda ndi kuchikana.ا
Tafseer
36.49
مَا يَنْظُرُونَ إِلَّا صَيْحَةً وَاحِدَةً تَأْخُذُهُمْ وَهُمْ يَخِصِّمُونَ
Ndithu, chimene akuyembekezera ndi Kuphulika kumodzi komwe kudzawagwira Mwadzidzidzi uku iwo akukangana (zadziko lapansi).ا
Tafseer
36.48
وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا الْوَعْدُ إِنْ كُنْتُمْ صَادِقِينَ
Ndipo akunena : “Kodi lonjezo ili, Lidzachitika liti, ngati mukunena Zoona?”ا
Tafseer
36.51
وَنُفِخَ فِي الصُّورِ فَإِذَا هُمْ مِنَ الْأَجْدَاثِ إِلَىٰ رَبِّهِمْ يَنْسِلُونَ
Ndipo lipenga lidzaimbidwa (loukitsa Akufa); iwo adzangozindikira Akutuluka m’manda kunka Kwa Mbuye wawo uku akuthamanga..ا
Tafseer
36.50
فَلَا يَسْتَطِيعُونَ تَوْصِيَةً وَلَا إِلَىٰ أَهْلِهِمْ يَرْجِعُونَ
Kenako sadzatha kupanga cholowa, kapena kubwerera ku mabanja awo.ا
Tafseer
36.53
إِنْ كَانَتْ إِلَّا صَيْحَةً وَاحِدَةً فَإِذَا هُمْ جَمِيعٌ لَدَيْنَا مُحْضَرُونَ
Kudzamveka phokoso limodzi lokha, ndipo adzaonekera kwa Ife onse pamodzi.ا
Tafseer
36.52
قَالُوا يَا وَيْلَنَا مَنْ بَعَثَنَا مِنْ مَرْقَدِنَا ۜ ۗ هَٰذَا مَا وَعَدَ الرَّحْمَٰنُ وَصَدَقَ الْمُرْسَلُونَ
Adzati: “Kalanga ife! Kodi Ndani watidzutsa pogona pathu?” (Adzawauza) “Izi ndi zimene Adalonjeza (Mulungu), Wachifundo Chambiri ndi zimene adanena Atumiki moona.”ا
Tafseer
36.55
إِنَّ أَصْحَابَ الْجَنَّةِ الْيَوْمَ فِي شُغُلٍ فَاكِهُونَ
Ndithu, anthu aku munda wa mtendere Lero akhala wotanganidwa ndi Chisangalalo.ا
Tafseer
36.54
فَالْيَوْمَ لَا تُظْلَمُ نَفْسٌ شَيْئًا وَلَا تُجْزَوْنَ إِلَّا مَا كُنْتُمْ تَعْمَلُونَ
“Ndipo mzimu uliwonse lero Suponderezedwa pa chilichonse. Ndipo mulipidwa pa zokhazo Munkachita.”ا
Tafseer
36.57
لَهُمْ فِيهَا فَاكِهَةٌ وَلَهُمْ مَا يَدَّعُونَ
M’menemo apeza (mtundu Uliwonse) wazipatso ndiponso Apeza chilichonse chimene Akuchifuna.ا
Tafseer
36.56
هُمْ وَأَزْوَاجُهُمْ فِي ظِلَالٍ عَلَى الْأَرَائِكِ مُتَّكِئُونَ
Iwo ndi akazi awo akhala M’mithunzi uku atatsamira mipando (Ya mtengo wapamwamba;)ا
Tafseer
36.61
وَأَنِ اعْبُدُونِي ۚ هَٰذَا صِرَاطٌ مُسْتَقِيمٌ
Koma kundipembedza Ine ndekha? Iyi ndi njira Yoongoka.ا
Tafseer
36.60
أَلَمْ أَعْهَدْ إِلَيْكُمْ يَا بَنِي آدَمَ أَنْ لَا تَعْبُدُوا الشَّيْطَانَ ۖ إِنَّهُ لَكُمْ عَدُوٌّ مُبِينٌ
Kodi sindidakulangizeni, E, inu Ana a Adamu kuti musapembedze Satana; ndithu, iye ndi mdani Woonekera kwa inu.ا
Tafseer
36.65
الْيَوْمَ نَخْتِمُ عَلَىٰ أَفْوَاهِهِمْ وَتُكَلِّمُنَا أَيْدِيهِمْ وَتَشْهَدُ أَرْجُلُهُمْ بِمَا كَانُوا يَكْسِبُونَ
Lero titseka kukamwa kwawo. Ndipo manja awo atiyankhula Ndipo miyendo yawo ichitira Umboni pa zomwe amachita.”ا
Tafseer
36.64
اصْلَوْهَا الْيَوْمَ بِمَا كُنْتُمْ تَكْفُرُونَ
Iloweni lero, chifukwa cha Kunkana kwanu (Mulungu).ا
Tafseer
36.67
وَلَوْ نَشَاءُ لَمَسَخْنَاهُمْ عَلَىٰ مَكَانَتِهِمْ فَمَا اسْتَطَاعُوا مُضِيًّا وَلَا يَرْجِعُونَ
Ndipo tikadafuna, tikadawasintha Kukhala ndi maonekedwe a nyama Pamalo pa wo pomwepo (pamene adali), Kotero kuti sakadatha kuyenda (Kunka patsogolo) ngakhale Kubwerera pambuyo.ا
Tafseer
36.66
وَلَوْ نَشَاءُ لَطَمَسْنَا عَلَىٰ أَعْيُنِهِمْ فَاسْتَبَقُوا الصِّرَاطَ فَأَنَّىٰ يُبْصِرُونَ
Ndipo tikadafuna, tikadafafaniza maso Awo; ndipo akadakhala akuthamangira njira; koma Akadapenya chotani?ا
Tafseer
36.69
وَمَا عَلَّمْنَاهُ الشِّعْرَ وَمَا يَنْبَغِي لَهُ ۚ إِنْ هُوَ إِلَّا ذِكْرٌ وَقُرْآنٌ مُبِينٌ
Ndipo sitidamphunzitse Ndakatulo, ndipo nkosayenera kwa lye . Qur’an Sichina, koma ndichikumbutso ndi Buku lomwe likulongosola Chilichonse.ا
Tafseer
36.68
وَمَنْ نُعَمِّرْهُ نُنَكِّسْهُ فِي الْخَلْقِ ۖ أَفَلَا يَعْقِلُونَ
Ndipo amene tikumtalikitsira moyo Wake, timam’bwezeranso pambuyo M’chilengedwe chake. Kodi bwanji saganizira Mwanzeru?ا
Tafseer
36.71
أَوَلَمْ يَرَوْا أَنَّا خَلَقْنَا لَهُمْ مِمَّا عَمِلَتْ أَيْدِينَا أَنْعَامًا فَهُمْ لَهَا مَالِكُونَ
Kodi saona kuti Ife tawalengera Nyama, m’zimene manja Athu akonza, Zomwe iwo akuti nzawo?ا
Tafseer
36.70
لِيُنْذِرَ مَنْ كَانَ حَيًّا وَيَحِقَّ الْقَوْلُ عَلَى الْكَافِرِينَ
Kuti awachenjeze amene ali moyo, Ndi kuti litsimikizike liwu (Lachilango) pa osakhulupirira.ا
Tafseer
36.73
وَلَهُمْ فِيهَا مَنَافِعُ وَمَشَارِبُ ۖ أَفَلَا يَشْكُرُونَ
Ndipo m’menemo muli ubwino ndi zakumwa zosiyana kwa iwo. Pamenepo, kodi iwo sadzayamikira?ا
Tafseer
36.72
وَذَلَّلْنَاهَا لَهُمْ فَمِنْهَا رَكُوبُهُمْ وَمِنْهَا يَأْكُلُونَ
Ndithudi, izi tawagonjera (Kuti azikwera) ena ndikudya nyama ya.ا
Tafseer
36.75
لَا يَسْتَطِيعُونَ نَصْرَهُمْ وَهُمْ لَهُمْ جُنْدٌ مُحْضَرُونَ
(Koma) siingathe kuwathandiza; Ndipo iwo ndi Asilikali amene akonzedwa Kulondera.ا
Tafseer
36.74
وَاتَّخَذُوا مِنْ دُونِ اللَّهِ آلِهَةً لَعَلَّهُمْ يُنْصَرُونَ
Ndipo adzipangira milungu (Yabodza) kusiya Mulungu (weniweni) Kuti athandizidwe nayo.ا
Tafseer
36.77
أَوَلَمْ يَرَ الْإِنْسَانُ أَنَّا خَلَقْنَاهُ مِنْ نُطْفَةٍ فَإِذَا هُوَ خَصِيمٌ مُبِينٌ
Kodi munthu sazindikira kuti Ife Tidamulenga ndi dontho la umuna? Koma iye wakhala Wotsutsa woonekera?ا
Tafseer
36.76
فَلَا يَحْزُنْكَ قَوْلُهُمْ ۘ إِنَّا نَعْلَمُ مَا يُسِرُّونَ وَمَا يُعْلِنُونَ
Mawu awo asakudandaulitse. Ndithu, Ife tikudziwa zimene Akubisa ndi zimene akuzionetsera Poyera.ا
Tafseer
36.79
قُلْ يُحْيِيهَا الَّذِي أَنْشَأَهَا أَوَّلَ مَرَّةٍ ۖ وَهُوَ بِكُلِّ خَلْقٍ عَلِيمٌ
Muuzeni: “Amene adawalenga poyamba adzawaukitsanso: lye Ngodziwa kulenga chilichonse.ا
Tafseer
36.78
وَضَرَبَ لَنَا مَثَلًا وَنَسِيَ خَلْقَهُ ۖ قَالَ مَنْ يُحْيِي الْعِظَامَ وَهِيَ رَمِيمٌ
Ndipo akutiponyera fanizo ndi kuiwala chilengedwe Chake. Akunena: “Ndani angaukitse Mafupa pomwe ali ofumbwa?”ا
Tafseer
36.81
أَوَلَيْسَ الَّذِي خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ بِقَادِرٍ عَلَىٰ أَنْ يَخْلُقَ مِثْلَهُمْ ۚ بَلَىٰ وَهُوَ الْخَلَّاقُ الْعَلِيمُ
Kodi Yemwe adalenga thambo ndi Nthaka (mukuganiza kuti) siwokhoza Kuwalenga (iwo kachiwiri) monga Momwe alili? Inde! Iye ndiMlengi Wamkulu, Wodziwa kwambiri!ا
Tafseer
36.80
الَّذِي جَعَلَ لَكُمْ مِنَ الشَّجَرِ الْأَخْضَرِ نَارًا فَإِذَا أَنْتُمْ مِنْهُ تُوقِدُونَ
Iye ndi Yemwe adakulengerani moto kuchokera kumtengo Wauwisi, womwe umayatsa nkhuni zanu.ا
Tafseer
36.83
فَسُبۡحَٰنَ ٱلَّذِي بِيَدِهِۦ مَلَكُوتُ كُلِّ شَيۡءٖ وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ
Kotero alemekezeke Yemwe m’manja Mwake muli ulamuliro pachinthu Chilichonse; ndipo kwa lye (ndiko) Mudzabwerera nonse.”ا
Tafseer
36.82
إِنَّمَا أَمْرُهُ إِذَا أَرَادَ شَيْئًا أَنْ يَقُولَ لَهُ كُنْ فَيَكُونُ
Akafuna chilichonse, Amangolamula kuti: “Khala”, ndipo chimachitikadi.ا
Tafseer
Chidule cha Surah Yaseen:
Surah Yaseen imatchedwa “Mtima wa Qur’an”. Nthawi zambiri amanenedwa kuti “Yaseen” ndi dzina la Mtumiki Muhammad (SAW). Ili ndi ma vesi 83 ndipo ndi mutu wa 36 wa Quran ndipo ili ndi mawu 807 ndi zilembo 3,028. Ili ndi ruku 5 (magawo). Ndi gawo la 22nd Juz ndipo ipitilira mpaka 23 Juz. Idavumbulutsidwa ku Makka, choncho imatchedwa Makki Surah ndipo ikutsindika mfundo zazikuluzikulu izi:
1. Kutsimikiza kwa Uneneri:
Surayi yayamba ndikunena za choonadi cha uthenga umene Mtumiki Muhammad (SAW) adaubweretsa. Yanenetsa kuti iye ndi mtumiki wotumidwa ndi Allah kuti atsogolere anthu.
2. Zizindikiro za Mulungu:
Surayi ikulozera zisonyezo zosonyeza kukhalapo kwa Allah ndi mphamvu zake kudzera mu chilengedwe. Yatchulanso za kusinthana kwa usiku ndi usana, kumera kwa zomera, ndi zodabwitsa za m’chilengedwe chonse, ndi kuwalimbikitsa anthu kuti azilingalira zizindikiro zimenezi monga umboni wa ukulu wa Allah.
3. Kukana Uthenga:
Likunena za kuuma khosi kwa anthu amene amakana uthengawo. Mosasamala kanthu za zisonyezo zowonekera ndi zozizwitsa zosonyezedwa kwa iwo, ambiri akupitirizabe kukana chowonadi, kufikitsa ku chilango chawo chosapeŵeka.
4. Zitsanzo za Mitundu Yakale:
Surayi yafotokoza za nkhani za anthu akale omwe adatsutsa Aneneri awo ndipo zotsatira zake adaonongeka. Izi ndi chenjezo kwa amene akutsutsa choonadi.
5. Kuuka ku imfa ndi Tsiku Lomaliza:
Surah Yaseen ikufotokoza za kuuka kwa akufa ndi moyo pambuyo pa imfa. Yatsindika kuti anthu onse adzaukitsidwa pa tsiku lachiweruzo, ndipo adzayankha mlandu pa zochita zawo.
6. Chifundo Chaumulungu:
Surayi yawatsimikizira okhulupirira za chifundo cha Allah ndi malipiro kwa amene akuvomereza uthengawo. Ikufotokozanso kusiyana pakati pa tsogolo la olungama ndi osakhulupirira, ndikugogomezera kuti okhulupirira adzakhala m’paradaiso.
7. Itanani Kuti Muganizire:
Surayi yamaliza ndi kuwalimbikitsa anthu kuti alingalire pa moyo wawo, zisonyezo za Mulungu zowazinga, ndi choonadi chenicheni chakuuka ku imfa ndi kuwerengera mlandu.